top of page

Malo Athu Okhala Kumwamba

1 Pakuti tidziwa kuti ngati msasa wathu wapadziko lapansi upasuka, tiri nao nyumba yocokera kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba. 2 Pakuti m’chihema ichi tibuula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu yakumwamba, 3 kuti ngati tingati povala ife tisapezeke amaliseche. 4 Pakuti pamene tikali m’chihemachi, tibuula, ndi kulemedwa, osati kuti tikufuna kuvula, koma kuti tibvalenso, kuti chakufacho chimezedwe ndi moyo. 5 Iye amene anatikonzekeretsa ife ku chinthu chomwecho ndi Mulungu, amene anatipatsa ife Mzimu monga chitsimikizo.

6 Choncho ndife olimba mtima nthawi zonse. Tidziwa kuti pokhala m’thupi, pokhala m’thupi, tiri kutali ndi Ambuye, 7 pakuti timayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. 8Inde, tiri olimbika mtima, ndipo tikonda kukhala kutali ndi thupi ndi kukhala kwathu ndi Ambuye. 9 Choncho, kaya tili kunyumba kapena kwina, timafunitsitsa kumusangalatsa. 10 Pakuti tonse tiyenera kuonekera kumpando woweruzira milandu wa Khristu, + kuti aliyense alandire zoyenera zimene anachita m’thupi, kaya zabwino kapena zoipa.

bottom of page